Musanalowe sacco, muyenera kudziwa zokhudza bungweli monga izi:
ZOSONKHA PA MWEZI
MADIPOSITI
Izi ndi ndalama zomwe membala amatha kusunga komanso kutapa ku sacco nthawi ina iliyonse angazifune.
MASHEYA
Mamembala onse amasonkha ndalama za umembala zosachepela K5,000.00 mwezi ndi mwezi. Ndalama yoyambira ndi K5,000.00
KUSANKHA OTENGA NDALAMA
a. Pofuna kulondoloza bwino lomwe kagawidwe ka ndalama za membala akamwalira, membala aliyense akuyenera kutchula munthu kapena anthu angapo oti adzalandire magawo a ndalama zomwe membalayo amasunga ku bungweli.
b. Membala atha kusintha maina a anthu odzalandira ndalamazi nthawi ina iliyonse malinga ndi momwe wafunira iye mwini.
INSHURANSI
Membala akamwalira, abale otsala amapatsidwa masheya onse. Insuransi imabweza ndalama zonse za ngongole ya omwalira ndipo otsala safunsidwanso kubweza ngongolezi. Komabe, inshuransiyi sigwira ntchito kwa mamembala omwe imfa yawo idabwera kamba kodzipha komanso ngati anali ataleka kulipira ngongoleyo pa nthawi ya imfa.
KUTULUKA BUNGWELI
Pamene membala akufuna kutuluka bungweli, ndondomeko izi zidzatsatidwa:
a. Membala adzapereka chidziwitso choti akufuna kutuluka SACCO cha nthawi yosachepera mwezi umodzi.
b. Potuluka bungweli, membala adzapereka chindapusa cha K1,000.00 chomwe chidzachoka ku masheya ake.
c. Masheya osatengedwa ku SACCO (Non Redeemable) adzagulitsidwa kwa membala wina ndipo membala wotulukayo adzalandira ndalamayo.